Fisi Sadzatheka

William Khalipwina Mpina

msilikaliyo adamugwira kholingo ndipo adalifinya molimbika. Fisi adalira chakwawo ndipo sadadzukenso.

Mbiri itamveka kuti Fisi waphedwa tidafuna kupeza yankho la uthenga wosazolowelekawo. Malingaliro adapotolozeka. Chimene chidakula pakati pathu kudali kusamvetsa, kuchita mantha ndi kuzunguzika. Zidachitika bwanji? Adali kuti iyeyo? Chuma chake sichidasakazike? Nanga mkazi wake pamodzi ndi ana adali bwanji? Kodi achipongwewo, adathawa kapena adagwidwa?
Fisi, atatembenuka mtima, adali munthu waulemu, wodziwa kulandira alendo komanso wokonda kupemphera. Mbiri yake yokonda kutolatola idaiwalika. Chimene tidachilandira ngakhale sitimachimvetsa chidali choti Fisi, monga momwe zimakhalira ndi anthu ena kuti amayamba kaye aphula njerwa zamoto kuti alemere, adangopezeka kuti ali ndi golosale yodzadza.
Mwanthawi zonse, Fisi adatuluka m’golosale mwake kuti akamulawire mkazi wake Nafisi kuti adali kupita ku ulendo wokaoda geni ku Nangantani. Nafisi adali kutsuka mbale kuseri kwa nyumba ndipo atamuona mwamuna wake adamuthamangira. Atanong’onezana, ulendo udayambika. Nthawi zambiri Fisi akamachoka, mkaziyo amatsala nkumagulitsa mu golosale koma sipamalephera awiri, atatu, omudandaula. Pakatha masiku atatu, pagolosalepo pamaima chigalimoto chodzadza ndi katundu. Pambuyo pake, Fisi amatulukira. Koma ulendo umenewu sizidayende choncho. Masiku anayi atapita, Nafisi adada nkhawa. Adakafunsa kwa anzake a Fisi omwe adapita nawo ku Nangantani koma aliyense adati sadamuone bwino mayendedwe ake.
Kenako NaFisi adapita kwa abusa kukafunsa koma abusa adati sadamve kanthu. Ali mkatikati mofunsirabe, anthu ena adamuuza Nafisi kuti ku ‘motchale’ ya ku Nangantani kudali mtembo wa mkulu wina umene sumadzindikiridwa. Iye adalibutsa liwiro la kumeneko. Atafika adapatsidwa mpata wokaona nkhope. Nafisi adatuluka m’menemo masayawa atasamba misozi. Adangofikira kuzigwetsa pansi.
Apolisi adamuuza Nafisi kuti pakati pa usiku, mmodzi mwa asilikali a ku Nangantani adamva phokoso la ndawala ndipo adaona mbava zinayi zitanyamula matumba a ndalama. Kuti aonetsetse, msilikaliyo adagona mphepete mwa nsewu ngati chiledzelele. Fisi atafika pamenepo adaima. Anzake aja adapitilira. Iye sadaupeze mtima. Adamugwedeza msilikaliyo kuti aone ngati adali moyo. Kenaka anatula pansi thumba lake ndipo adamutembenuza msilikaliyo kuti amubere mfuti. Nthawi yomweyo, msilikaliyo adamugwira kholingo ndipo adalifinya molimbika. Fisi adalira chakwawo ndipo sadadzukenso.