BULU SAGANIZA

Nthano by Dyson Gonthi

Mkango Ndi chirombo choopsa ndipo zirombo zambiri zikauona zimathawa kuopa kuti zingaphedwe.

Kalekale mkango wina unakalamba kwambiri motero kuti umalephera kugwira nyama kuti udye. Pachifukwa chimenechi kawiri kawiri mkangowo umakhala ndi njala.

Tsiku lina mkangowo utakhalakhala udaganiza kulemba ntchito nkhandwe kuti nkhandweyo izigwira nyama kuti mkangowo usamavutike. Nkhandweyo poyamba idaganiza kuti mkangowo udafuna kuti uphe ndi kudya  nkhandweyo koma zinthu sizidali choncho.  Iwo unkafuna kuti nkhandweyo iziphera mkangowo chakudya.

Mkangowo udafotokozera nkhandweyo kuti iwo wafuna kulemba nkhandweyo chifukwa ndi yochenjera komanso ndi yaliwiro. Nkhandwe idavomera kulembedwa ntchitoyo Ndipo nkhandweyo idavomeradi kugwira ntchitoyo pa udindo wake ngati nduna.

Nkhandwe idayamba kugwira ntchito yake bwinobwino kumakagwira nyama zina kumadera ena nkudzapereka kwa mkangowo. Pachifukwa chimenechi mkango uja sumavutikanso chakudya.

Tsiku lina nkhandwe ili kusakasaka mtchire idakumana ndi Bulu.  Poti bulu ndi wa mphamvu chomwe nkhandwe idachita ndi kunamiza buluyo kuti mkango ukumufuna kuti akhale mlangizi wake wa mkangowo. Pomva zomwe nkhandwe idanena bulu adakana kwa ntuwa galu kuti alowe ntchitoyo. Iye adati sizoona koma kuti mkangowo ukufuna kudya buluyo.

Komabe nkhandwe idayesetsa kunyengerera buluyo kuti asaope ndipo kwa mkangowo azikakhala mosangalala.  Chifukwa chomunyengerera kenako bulu adavomera.

Ananyamuka limodzi ndi kukafika kwa mkango, mkangowo powona udatcha dobvu chifukwa idali nyama imene umayifuna kwambiri.

Buluyo atangoyandikira pango’ono, potinso mkangowo udali ndi njara, sudachedwe udamubwandira bulu uja. Mwa mwayi Bulu adafwamphuka ndi kuthawa koma akunjenjemera kuti adakafa.

Malinga ndi zomwe zidachitikazo nkhandwe idadzudzula mkangowo chifukwa chofulumira kumbwandira Bulu uja mmalo moti ukadayamba wa munyengerera bwino. Chifukwa cha mtima wa phamphu komanso njara ndi njara udamulephera Bulu wofikafika.

Khaleni Khaleni nkhandwe ija idakomananso ndi Bulu uja.  Atakumana adayamba kudzudzulana chifukwa cha chiwembu chija. Koma nkhandwe mwa kuchenjera idalangiza Buluyo kuti sadakayenera kuthawa .Mkango udamudumphira chifukwa udali okondwa kumuona ndikuti wapeza bwenzi umalifuna kwambiri.

Tsoka ilo, Bulu uja adanyengekanso ndikupitiriranso limodzi kwa mkangowo. Ndipo onse atafika nkhandwe idakhalira pambuyo ndipo mwamwayi mkango sudapupulume. kenaka mkango udangoti pa khosi la bulu gwi, basi Bulu adafera pomwepo.

Mkango kuti uziyamba kudya nkhandwe idauza mkangowo kuti kudya osasamba sikwabwino, Nkhandwe idauza mkangowo kuti ukasambe ndipo ilondera nyamayo. Mkango utapita kumtsinje nkhandwe idagogomola mutu wa Bulu nkudyamo bongobose kenako idavundikira mutuwo bwinobwino osaonekanso kuti ndi osweka.

Nkhandwe idathamangira kudya bongobo chifukwa imaukonda koposa ziwalo zina zonse za nyama ya bulu.

Mkango utamaliza kusamba, naonso maganizo ake adali woti uyambe kudya bongo. Utafika udathokoza nkhandweyo chifukwa udali ndi thukuta polimbana  ndi Bulu uja koti kunali kwabwino kuyamba kukasamba. Kenako udayesa kuswa mutu uja ndipo sudavutike  chifukwa mutuwo unali utasweka kale. Koma powona sudapezemo bongo, mkango mopsa mtima udafusa nkhandwe  kuti bongo buli kuti. Poyankha nkhandwe idauza mkangowo kuti Bulu sakhala ndi Bongo, ndipo nkhandwe idati kudakakhala kuti Bulu amakhala ndi bongo sakadabwereranso kwa mkangowo.

Ndi chifukwa chake nkhandwe imati bulu alibe bongo.

Ndipo ndi mmene nkhandweyo idafotokozera za nkhaniyi mkango udafika pogoma ndi kukhulupirira kuti zowona buluyo sakadabvomera kubweranso.

Mkango udavomereza pokumbukira mawu aja woti, mphechepeche mwa njobvu sadutsamo kawiri.